Ecclesiastes 2:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja nthaŵi zina munthu amene wagwira ntchito zolemetsa mwaluntha, mwanzeru ndi mwaluso, zonsezo ayenera kuzisiyira munthu amene sadakhetserepo konse thukuta, kuti akondwere nazo. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo nzoipa kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti pali munthu wina agwira ntchito mwanzeru ndi modziwa nadzipinduliramo; koma adzapereka gawo lake kwa munthu amene sanagwirepo ntchito. Ichinso ndi chabe ndi choipa chachikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti munthu atha kugwira ntchito yake mwanzeru, chidziwitso ndi luntha, ndipo kenaka nʼkusiyira wina amene sanakhetserepo thukuta. Izinso ndi zopandapake ndiponso tsoka lalikulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti pali munthu wina agwira nchito mwanzeru ndi modziwa nadzipinduliramo; koma adzapereka gawo lace kwa munthu amene sanagwirapo nchito. Icinso ndi cabe ndi coipa cacikuru.