Ecclesiastes 2:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kwa munthu palibe chabwino china choposa kudya, kumwa ndi kukondwerera ntchito zake. Ngakhale zimenezi ndazindikira kuti nzochokera kwa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi si chabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m'ntchito yake? Ichinso ndinachizindikira kuti chichokera kudzanja la Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa munthu palibe chabwino china kuposa kudya, kumwa ndi kukondwerera ntchito zake. Izinso ndaona kuti ndi zochokera kwa Mulungu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi si cabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wace, zabwino m'nchito yace? icinso ndinacizindikira kuti cicokera ku dzanja la Mulungu.