Ecclesiastes 2:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu munthu wokondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamsandutsa waluntha, wanzeru ndi wosangalala. Koma wochimwa amampatsa ntchito yokunkha ndi younjika zinthu, kenaka zonsezo nkuzipatsa munthu wokondwetsa Mulungu. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi chidziwitso ndi chimwemwe; koma wochimwa amlawitsa vuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu amene amakondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamusandutsa wanzeru, wozindikira ndi wachisangalalo, koma wochimwa, Mulungu amamupatsa ntchito yosonkhanitsa ndi kusunga chuma kuti adzachipereke kwa amene Mulunguyo amakondwera naye. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi cidziwitso ndi cimwemwe; koma wocimwa amlawitsa bvuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Icinso ndi cabe ndi kungosautsa mtima.