Ecclesiastes 2:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaadzikundikiranso siliva ndi golide ndiponso chuma chochokera kwa mafumu amene ndinkaŵalamulira. Ndinali ndi ondiimbira nyimbo, amuna ndi akazi omwe. Ndinalinso ndi akazi aang'ono ochuluka, aja amasangalatsa mitima ya amunaŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndinakundikanso siliva ndi golide ndi chuma cha mafumu ndi madera a dziko; ndinaitanitsa amuna ndi akazi akuimba ndi zokondweretsazo za ana a anthu, ndizo zoimbira za mitundumitundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinadzikundikira siliva ndi golide, ndiponso chuma chochokera kwa mafumu ndi madera awo. Ndinali ndi amuna ndi akazi oyimba ndiponso azikazi; zinthu zokondweretsa mtima wa munthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndinakundikanso siliva ndi golidi ndi cuma ca mafumu ndi madera a dziko; ndinaitanitsa amuna ndi akazi akuyimba ndi zokondweretsazo za ana a anthu, ndizo zoyimbira za mitundu mitundu.