Ecclesiastes 3:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikudziŵa kuti zimene Mulungu amazichita zimakhazikika mpaka muyaya. Palibe zimene zingathe kuwonjezedwa kapena kuchotsedwapo pa zimenezo. Mulungu adazipanga motero, kuti choncho anthu azimumvera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidziwa kuti zonse Mulungu azichita zidzakhala kufikira nthawi zonse; sungaonjezepo kanthu, ngakhale kuchotsapo; Mulungu nazichita kuti anthu akaope pamaso pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikudziwa kuti chilichonse chimene Mulungu amachita chidzakhala mpaka muyaya; palibe zimene zingawonjezedwe kapena kuchotsedwa. Mulungu amazichita kuti anthu azimuopa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidziwa kuti zonse Mulungu azicita zidzakhala kufikira nthawi zonse; sungaonjezepo kanthu, ngakhale kucotsapo; Mulungu nazicita kuti anthu akaope pamaso pace.