Ecclesiastes 3:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
China chimene ndidachiwona pansi pano ndi ichi: Koyenera kukhala chiweruzo chabwino, komwekonso kumapezeka kuipa mtima. Koyenera kukhala chilungamo, komwekonso kumapezeka zoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso ndinaona kunja kuno malo akuweruza, komweko kuli zoipa; ndi malo a chilungamo, komweko kuli zoipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndinaona chinthu chinanso pansi pano: ku malo achiweruzo, kuyipa mtima kuli komweko, ku malo achilungamo, kuyipa mtima kuli komweko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso ndinaona kunja kuno malo akuweruza, komweko kuli zaipa; ndi malo a cilungamo, komweko kuli zoipa.