Ecclesiastes 3:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene zimachitikira anthu, zomwezonso zimachitikira nyama. Monga chinacho chimafa, chinacho chimafanso. Zonsezo zimapuma mpweya umodzimodzi, munthu saposa nyama. Zonsezi nzopandapake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera nchimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi chabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimene zimachitikira munthu, zomwezonso zimachitikira nyama; chinthu chimodzi chomwecho chimachitikira onse: Monga munthu amafa momwemonso nyama imafa. Zonsezi zimapuma mpweya umodzimodzi omwewo; munthu saposa nyama. Zonsezi ndi zopandapake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti comwe cigwera ana a anthu cigweranso nyamazo; ngakhale cowagwera ncimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi cabe,