Ecclesiastes 3:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho ndidaona kuti palibe chinthu chabwino kuposa kuti munthu azikondwerera ntchito yake, pakuti chake chenicheni nchimenechi. Ndani angathe kudziŵa chimene chidzamchitikire iye atafa?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mwemo ndinazindikira kuti kulibe kanthu kabwino kopambana aka, kuti munthu akondwere ndi ntchito zake; pakuti gawo lake ndi limeneli; pakuti ndani adzamfikitsa kuona chomwe chidzachitidwa atafa iyeyo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero ndinaona kuti palibe chinthu chabwino kwa munthu kuposa kuti munthu azisangalala ndi ntchito yake, pakuti ichi ndiye chake chenicheni. Pakuti ndani amene angamubweretse kuti adzaone zimene zidzamuchitikira iye akadzamwalira?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mwemo ndinazindikira kuti kulibe kanthu kabwino kopambana aka, kuti munthu akondwere ndi nchito zace; pakuti gawo lace ndi limeneli; pakuti ndani adzamfikitsa kuona comwe cidzacitidwa ataca iyeyo?