Ecclesiastes 4:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaonanso kuzunza kulikonse kochitika pansi pano. Ndipo ndidaona ozunzidwa akulira misozi, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti aŵatonthoze. Panalibe oŵatonthoza chifukwa ozunzawo anali ndi mphamvu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinayangʼananso ndi kuona chipsinjo chimene chimachitika pansi pano: ndinaona misozi ya anthu opsinjika, ndipo iwo alibe owatonthoza; mphamvu zinali ndi anthu owapsinjawo ndipo iwonso analibe owatonthoza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimacitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.