Ecclesiastes 4:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndinkaganiza za anthu onse amene amakhala pansi pano, ndipo ndidazindikira kuti pakati paopo panali mnyamata uja amene anali wodzatenga malo a mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinapenyera anthu onse amoyo akuyenda kunja kuno, kuti anali ndi mwana, wachiwiri, amene adzalowa m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndinaona kuti iwo onse amene anakhala ndi moyo ndi kuyenda pansi pano anatsatira wachinyamatayo, amene anatenga malo a mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinapenyera anthu onse amoyo akuyenda kunja kuno, kuti anali ndi mwana, waciwiri, amene adzalowa m'malo mwace.