Ecclesiastes 4:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panali munthu amene anali yekha, wopanda mwana kapena mbale, komabe ntchito yake yolemetsa sinkatha. Maso ake sankakhutitsidwa nacho chuma chake. Motero sankadzifunsa konse kuti, “Kodi ntchito yolemetsa ndikuigwirayi ndiponso mavuto a kudzimana zokondweretsaŵa, ndikuchitira yani?” Zimenezi nzopanda phindu ndiponso nzosakondweretsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Panali munthu amene anali yekhayekha; analibe mwana kapena mʼbale. Ntchito yake yolemetsa sinkatha, ndipo maso ake sankakhutitsidwa ndi chuma chake. Iye anadzifunsa kuti, “Kodi ntchito yosautsayi ndikuyigwirira yani? Nanga nʼchifukwa chiyani ndikudzimana chisangalalo?” Izinso ndi zopandapake, zosasangalatsa!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pali mmodzi palibe waciwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma nchito yace yonse iribe citsiriziro, ngakhale diso lace silikhuta cuma. Samati, Ndigwira nchito ndi kumana moyo wanga zabwino cifukwa ca yani? Icinso ndi cabe, inde, bvuto lalikuru.