Ecclesiastes 5:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uzisamala mayendedwe ako ukamapita ku Nyumba ya Mulungu. Kuli bwino kupita kumeneko kukaphunzirako, kupambana kukangopereka nsembe chabe ngati anthu opusa, amene sadziŵa kuti akuchita zoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Samalira phazi lako popita kunyumba ya Mulungu; pakuti kuyandikira kumvera kupambana kupereka nsembe za zitsiru; pakuti sizizindikira kuti zilikuchimwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uzisamala mayendedwe ako pamene ukupita ku nyumba ya Mulungu. Upite pafupi kuti ukamvetsere mʼmalo mopereka nsembe ya zitsiru zimene sizizindikira kuti zikuchita zolakwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Samalira phazi lako popita ku nyumba ya Mulungu; pakuti kuyandikira kumvera kupambana kupereka nsembe za zitsiru; pakuti sizizindikira kuti zirikucimwa.