Ecclesiastes 5:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwina Mulungu amamlemeretsa munthu pakumpatsa chuma ndi zabwino zina, namlola kuti akondwerere zonsezo. Munthuyo azilandire zimenezo ndi kumakondwerera ntchito zake zonse zolemetsa. Imeneyi ndi mphatso yochokeradi kwa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inde yemwe Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma, namninkhanso mphamvu ya kudyapo, ndi kulandira gawo lake ndi kukondwera ndi ntchito zake; umenewu ndiwo mtulo wa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komatu pamene Mulungu apereka chuma kwa munthu aliyense ndi zinthu zina, ndi kulola kuti akondwere ndi chumacho, munthuyo alandire chumacho ndi kusangalala ndi ntchito yake, imene ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inde yemwe Mulungu wamlemeretsa nampatsa cuma, namninkhanso mphamvu ya kudyapo, ndi kulandira gawo lace ndi kukondwera ndi nchito zace; umenewu ndiwo mtulo wa Mulungu.