Ecclesiastes 5:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ukalumbira chinthu kwa Mulungu, usachedwe kuchichita, chifukwa Mulungu sakondwera nazo zitsiru. Zimene wazilumbira, uzichitedi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Utawinda chiwindo kwa Mulungu, usachedwe kuchichita; pakuti sakondwera ndi zitsiru; chita chomwe unachiwindacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene ulumbira kwa Mulungu usachedwe kukwaniritsa chimene walumbiracho. Iye sakondweretsedwa ndi chitsiru; kwaniritsa lumbiro lako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Utawinda ciwindo kwa Mulungu, usacedwe kucicita; pakuti sakondwera ndi zitsiru; cita comwe unaciwindaco.