Ecclesiastes 5:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakamwa pako pasakuchimwitse, kuti choncho usayenerenso kukauza wansembe wa Mulungu kuti, “Ai, ndinkangonena!” Chifukwa chiyani ufuna kuputa Mulungu? Kodi ukufuna kuti aononge zimene wazigwirira ntchito?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usalole m'kamwa mwako muchimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako chifukwa ninji, naononge ntchito ya manja ako?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakamwa pako pasakuchimwitse. Ndipo usanene kwa mthenga wa mʼNyumba ya Mulungu kuti, “Ndinalakwitsa polumbira.” Chifukwa chiyani ukufuna Mulungu akwiye ndi mawu ako ndiponso ntchito ya manja ako?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usalole m'kamwa mwako mucimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako cifukwa ninji, naononge nchito ya manja ako?