Ecclesiastes 5:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ukamaona anthu osauka akuzunzika m'dziko, ndiponso anthu ena akupsinja anzao ndi kuŵalanda ufulu wao mwankhanza, usadabwe nazo zimenezo. Paja woyang'anira wokulapo ali naye wina wamkulu kwambiri amene amamuyang'anira. Ndipo palinso akuluakulu enanso oyang'anira iwowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati uwona anthu osauka akuzunzika mʼdziko, ndiponso anthu ena akupsinja anzawo ndi kuwalanda ufulu wawo, usadabwe ndi zinthu zimenezi; pakuti woyangʼanira ali naye wina womuyangʼanira wamkulu, ndipo pamwamba pa awiriwa pali ena akuluakulu owaposa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kucotsa cilungamo ndi ciweruzo mwaciwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkuru wopambana asamalira; ndipo alipo akuru ena oposa amenewo.