Ecclesiastes 6:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndani amadziŵa zomkomera munthu kwenikweni pa nthaŵi yochepa imene munthuyo ali ndi moyo? Moyo wake ndi wa masiku ochepa, ndi wopandapake, umangopitirira ngati mthunzi. Ndani angathe kumufotokozera munthuyo zimene zidzachitike pansi pano iyeyo atafa?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ndani amene amadziwa chomwe ndi chabwino pa moyo wa munthu, pakuti moyo wake ndi wa masiku ochepa ndi opandapake, umangopitira ngati mthunzi. Ndani amene angamufotokozere zimene zidzachitika pansi pano iye atapita?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndani adziwa comwe ciri cabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wace wacabe umene autsiriza ngati mthunzi? pakuti ndani adzauza munthu cimene cidzaoneka m'tsogolo mwace kunja kuno?