Ecclesiastes 6:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu kukulemeretsa, kukupatsa chuma ndi ulemu, osasoŵa kanthu kalikonse kamene ukukalakalaka, koma tsono osakupatsa mwai woti udyerere zinthuzo, wodyerera nkukhala munthu wachilendo. Zimenezi nzothetsa nzeru, ndipo ndi vuto lokhumudwitsa kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma ndi ulemu, mtima wake susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ichi ndi chabe ndi nthenda yoipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu amapereka chuma, zinthu ndi ulemu kwa munthu, kotero kuti munthuyo sasowa kanthu kalikonse kamene akukalakalaka, koma Mulungu samulola kuti adyerere zinthuzo, ndipo mʼmalo mwake amadyerera ndi mlendo. Izi ndi zopandapake, ndi zoyipa kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa cuma ndi ulemu, mtima wace susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ici ndi cabe ndi nthenda yoipa,