Ecclesiastes 7:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uzikondwa mwai ukakufikira, ndipo tsoka likakugwera uzilingalirapo bwino pamenepo. Udziŵe kuti ndi Mulungu yemwe amene amatumiza mwai ndi tsoka. Amatero kuti munthu asadziŵiretu zimene zidzachitike m'tsogolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku la mwai kondwera, koma tsiku la tsoka lingirira; Mulungu waika ichi pambali pa chinzake, kuti anthu asapeze kanthu ka m'tsogolo mwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene zinthu zili bwino, sangalala; koma pamene zinthu sizili bwino, ganizira bwino: Mulungu ndiye anapanga nthawi yabwinoyo, ndiponso nthawi imene si yabwinoyo. Choncho munthu sangathe kuzindikira chilichonse cha mʼtsogolo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku la mwai kondwera, koma tsiku la tsoka lingirira; Mulungu waika ici pambali pa cinzace, kuti anthu asapeze kanthu ka m'tsogolo mwao.