Ecclesiastes 7:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuli bwino kupita ku nyumba yamaliro kupambana kupita ku nyumba yamadyerero. Pakuti imfa ndiye mathero ake a anthu onse, tsono amoyo azisinkhasinkha bwino zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kunka kunyumba ya maliro kupambana kunka kunyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuli bwino kupita ku nyumba yamaliro kusiyana ndi kupita ku nyumba yamadyerero: Pakuti imfa ndiye mathero a munthu aliyense; anthu amoyo azichisunga chimenechi mʼmitima mwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kunka ku nyumba ya maliro kupambana kunka ku nyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo.