Ecclesiastes 7:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero ndidaikapo mtima kwambiri kuti ndidziŵe, ndifufuze ndi kumafunafuna nzeru ndi m'mene zinthu zimakhalira. Ndidafunanso kumvetsa kuipa kwake kwa uchitsiru ndiponso kupusa kwake kwa msala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udyo ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero ndinayikapo mtima wanga kuti ndidziwe, ndifufuze ndi kumafunafuna nzeru ndi mmene zinthu zimakhalira ndipo ndinafunanso kudziwa kuyipa kwa uchitsiru ndiponso kupusa kwake kwa misala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udio ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;