Ecclesiastes 7:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidapeza china choŵaŵa kupambana imfa. Chinthucho ndi mkazi amene ali ngati msampha, amene mtima wake uli ngati ukonde, ndipo manja ake ali ngati maunyolo. Munthu wokondweretsa Mulungu amamthaŵa mkaziyo, koma wochimwa amalolera kukhala kapolo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wake ukunga maukonde, manja ake ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wochimwa adzagwidwa naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinapeza kanthu kowawa kupambana imfa, mkazi amene ali ngati khoka, amene mtima wake uli ngati khwekhwe, ndipo manja ake ali ngati maunyolo. Munthu amene amakondweretsa Mulungu adzathawa mkaziyo, koma mkaziyo adzakola munthu wochimwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wace ukunga maukonde, manja ace ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wocimwa adzagwidwa naye.