Ecclesiastes 7:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidapeza chokhachi chakuti Mulungu pomulenga munthu, adampatsa mtima wolungama, koma anthu amatsata njira zaozao zambirimbiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, ichi chokha ndachipeza kuti Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundumitundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chokhacho chimene ndinachipeza ndi ichi: Mulungu analenga munthu, anamupatsa mtima wolungama, koma anthu anatsatira njira zawozawo zambirimbiri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, ici cokha ndacipeza kuti Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundu mitundu.