Ecclesiastes 8:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndani angafanefane ndi munthu wanzeru? Ndani angadziŵe kutanthauza zinthu? Munthu nzeru zake zimampatsa chimwemwe, ndipo ukali umachoka pankhope pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndani akunga wanzeru? Ndani adziwa tanthauzo la mau? Nzeru ya munthu iwalitsa nkhope yake, kuduwa kwa nkhope yake ndi kusanduka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndani angafanane ndi munthu wanzeru? Ndani angadziwe kutanthauzira zinthu? Nzeru imabweretsa chimwemwe pa nkhope ya munthu ndipo imasintha maonekedwe ake awukali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndani akunga wanzeru? Ndani adziwa tanthauzo la mau? Nzeru ya munthu iwalitsa nkhope yace, kuduwa kwa nkhope yace ndi kusanduka.