Ecclesiastes 8:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ndidaona oipa akuikidwa m'manda. Iwowo kale ankaloŵa ndi kumatuluka m'malo oyera, ndipo mumzindamo anthu ankaŵatamanda m'mene ankachita zinthu zoterezi. Zimenezinso nzachabechabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinaona oipa alikuikidwa m'manda ndi kupita; ndipo omwe anachita zolungama anachokera kumalo opatulika akumudzi nawaiwala; ichinso ndi chabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka, ndinaona anthu oyipa akuyikidwa mʼmanda, iwo amene ankalowa ndi kumatuluka mʼmalo opatulika ndipo ankatamandidwa mu mzindawo pamene ankachita zimenezi. Izinso ndi zopandapake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaona oipa alikuikidwa m'manda ndi kupita; ndipo omwe anacita zolungama anacokera ku malo opatulika a ku mudzi nawaiwala; icinso ndi cabe.