Ecclesiastes 8:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale kuti wochimwa amati akachita zoipa kambirimbiri, amakhalabe moyo nthaŵi yaitali, komabe ndikudziŵa kuti omvera Mulungu ndiwo amene zinthu zidzaŵayendere bwino, poti ndi amene amamlemekeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Angakhale wochimwa achita zoipa zambirimbiri, masiku ake ndi kuchuluka, koma ndidziwitsadi kuti omwe aopa Mulungu naopa pamaso pake adzapeza bwino;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale munthu woyipa apalamule milandu yambirimbiri, nʼkumakhalabe ndi moyo wautali, ine ndikudziwa kuti anthu owopa Mulungu zinthu zidzawayendera bwino, omwe amapereka ulemu pamaso pa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Angakhale wocimwa acita zoipa zambirimbiri, masiku ace ndi kucuruka, koma ndidziwitsadi kuti omwe aopa Mulungu naopa pamaso pace adzapeza bwino;