Ecclesiastes 8:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pali chinthu china chachabechabe chimene chimachitika pansi pano. Chinthucho ndi ichi: mwina anthu abwino amalangidwa ngati ochita zoipa, pamene oipa amalandira zabwino ngati kuti ndi anthu abwino. Ndikuti zimenezinso nzachabechabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pali chinthu chachabe chimachitidwa pansi pano; chakuti alipo olungama amene aona zomwe ziyenera ntchito za oipa, ndipo alipo oipa amene aona zomwe ziyenera ntchito za olungama. Ndinati, Ichinso ndi chabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palinso chinthu china chopanda phindu chomwe chimachitika pa dziko lapansi: anthu olungama amalangidwa ngati anthu osalungama. Pamene oyipa amalandira zabwino ngati kuti ndi anthu abwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pali cinthu cacabe cimacitidwa pansi pano; cakuti alipo olungama amene aona zomwe ziyenera nchito za oipa, ndipo alipo oipa amene aona zomwe ziyenera nchito za olungama, Ndinati, Icinso ndi cabe.