Ecclesiastes 8:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ndidaona ntchito zonse za Mulungu. Palibe munthu amene angathe kuzitulukira zonse zimene zimachitika pansi pano. Ngakhale munthu ayesetse chotani kuzimvetsa, sadzafikapo. Ngakhale munthu wanzeru anene kuti akudziŵa zinthu, nkosatheka kuti azitulukire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo ndinaona ntchito zonse za Mulungu kuti anthu sangalondole ntchito zichitidwa pansi pano; pakuti angakhale munthu ayesetsa kuzifunafuna koma sadzazipeza; indetu ngakhalenso wanzeru akati, ndidziwa, koma adzalephera kuzilondola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamenepo ndinaona zonse zimene Mulungu anazichita. Palibe munthu amene angathe kuzimvetsa zonse zimene zimachitika pansi pano. Ngakhale munthu ayesetse kuzifufuza, sangathe kupeza tanthauzo lake. Ngakhale munthu wanzeru atanena kuti iye amadziwa, sangathe kuzimvetsetsa zinthuzo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo ndinaona nchito zonse za Mulungu kuti anthu sangalondole nchito ziciddwa pansi pano; pakuti angakhale munthu ayesetsa kuzifunafuna koma sadzazipeza; indetu ngakhalenso wanzeru akati, ndidziwa, koma adzalephera kuzilondola.