Ecclesiastes 9:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zonse ndanenazi ndidazilingalirapo, ndipo ndidatsimikiza kuti anthu ochita chilungamo ndi anthu anzeru ali m'manja mwa Mulungu pamodzi ndi ntchito zao zomwe. Koma palibe munthu angadziŵe zimene zili m'tsogolo mwake, ngakhale zikhale za chikondi, kapena za chidani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti zonsezi ndinazisunga mumtima ndikalondoletu zonsezi; kuti olungama ndi anzeru ndi ntchito zao ali m'manja a Mulungu; ngakhale kukonda ngakhale kudana anthu sadziwa; zonse zili m'tsogolo mwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinalingalira zonse ndanenazi ndipo ndinapeza kuti anthu olungama ndi anthu anzeru ali mʼmanja mwa Mulungu pamodzi ndi zimene amachita, koma palibe amene amadziwa zimene zikumudikira mʼtsogolo mwake, kaya chikondi kapena chidani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti zonsezi ndinazisunga mumtima ndikalondoletu zonsezi; kuti olungama ndi anzeru ndi nchito zao ali m'manja a Mulungu; ngakhale kukonda ngakhale kudana anthu sadziwa; zonse ziri m'tsogolo mwao.