Ecclesiastes 9:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaonanso pansi pano kuti opambana pa kuthamanga si aliŵiro okhaokha, opambana pa nkhondo si amphamvu okhaokha, ndiponso okhala ndi chakudya si anzeru okhaokha. Olemera si odziŵa zambiri okhaokha, ndipo si anthu aluso okhaokha amene anzao amaŵakomera mtima. Onsewo mwai umangoŵagwera pa nthaŵi yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe atamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinaonanso chinthu china pansi pano: opambana pa kuthamanga si aliwiro, kapena opambana pa nkhondo si amphamvu, ndiponso okhala ndi chakudya si anzeru, kapena okhala ndi chuma si odziwa zambiri, kapena okomeredwa mtima si ophunzira; koma mwayi umangowagwera onsewa pa nthawi yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe atamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwace.