Ecclesiastes 9:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kungoti munthu saidziŵa nthaŵi yake. Monga momwe nsomba zimagwidwira mu ukonde, monga momwenso mbalame zimakodwera mu msampha, anthunso nchimodzimodzi. Amachita ngati kukodwa mu msampha pa nthaŵi yoipa, pamene tsoka laŵagwera mwadzidzidzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti munthu sadziwatu mphindi yake; monga nsomba zigwidwa m'ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthawi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kungoti palibe munthu amene amadziwa kuti nthawi yake idzafika liti: monga momwe nsomba zimagwidwira mu ukonde, kapena mmene mbalame zimakodwera mu msampha, chimodzimodzinso anthu amakodwa mu msampha pa nthawi yoyipa, pamene tsoka limawagwera mosayembekezera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti munthu sadziwatu mphindi yace; monga nsomba zigwidwa m'ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthawi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.