Ecclesiastes 9:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mumzindamo munali munthu wina wosauka koma wanzeru. Munthu ameneyo adaupulumutsa mzindawo ndi nzeru zakezo. Komabe panalibe ndi mmodzi yemwe amene adamkumbukira wosaukayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma anapezedwamo mwamuna wanzeru wosauka, yemweyo napulumutsa mudziwo ndi nzeru yake; koma panalibe anthu anakumbukira wosauka ameneyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mu mzindamo munali munthu wosauka koma wanzeru, ndipo anapulumutsa mzindawo ndi nzeru zakezo. Koma palibe amene anakumbukira munthu wosaukayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma anapezedwamo mwamuna wanzeru wosauka, yemweyo napulumutsa mudziwo ndi nzeru yace; koma panalibe anthu anakumbukira wosauka ameneyo.