Ecclesiastes 9:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye ine ndikuti nzeru nzabwino ndithu kupambana mphamvu, ngakhale kuti anthu sazimvera nzeru za munthu wosauka, ndipo za mau ake salabadako nkomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ndinati, Nzeru ipambana mphamvu; koma anyoza nzeru ya wosauka, osamvera mau ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ine ndinati, “Nzeru ndi yopambana mphamvu.” Koma nzeru ya munthu wosauka imanyozedwa, ndipo palibe amene amalabadirako za mawu ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ndinati, Nzeru ipambana mphamvu; koma anyoza nzeru ya wosauka, osamvera mau ace.