Ecclesiastes 9:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu onse zimene zidzaŵaonekere nzimodzimodzi, ochita chifuniro cha Mulungu ndi okana omwe, abwino ndi oipa, osamala zachipembedzo ndi osasamala omwe, opereka nsembe ndi osapereka omwe. Wabwino amafanafana ndi woipa. Wochita malumbiro amafanafana ndi woopa kulumbira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zonse zigwera onse chimodzimodzi; kanthu kamodzi kangogwera wolungama ndi woipa; ngakhale wabwino ndi woyera ndi wodetsedwa; ngakhale wopereka nsembe ndi wosapereka konse; wabwino alingana ndi wochimwa; wolumbira ndi woopa lumbira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onsewa mathero awo ndi amodzi, anthu olungama ndi anthu oyipa, abwino ndi oyipa, oyera ndi odetsedwa, amene amapereka nsembe ndi amene sapereka nsembe. Zomwe zimachitikira munthu wabwino, zimachitikiranso munthu wochimwa, zomwe zimachitikira amene amalumbira, zimachitikiranso amene amaopa kulumbira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zonse zigwera onse cimodzimodzi; kanthu kamodzi kangogwera wolungama ndi woipa; ngakhale wabwino ndi woyera ndi wodetsedwa: ngakhale wopereka nsembe ndi wosapereka konse; wabwino alingana ndi wocimwa; wolumbira ndi woopa lumbiro.