Ecclesiastes 9:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimene chili choipa kwambiri mwa zonse zochitika pansi pano ndi ichi chakuti tsoka limodzimodzi limagwera onse. Chinanso nchakuti mitima ya anthu njodzaza ndi zoipa. M'mitima mwao mumadzaza ndi zamisala pamene ali moyo, pambuyo pake kwao nkufa ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choyipa chimene chili mʼzonse zochitika pansi ndi ichi: Mathero a zonse ndi amodzi. Ndithu, mitima ya anthu ndi yodzaza ndi zoyipa, ndipo mʼmitima mwawo muli zamisala pamene ali ndi moyo, potsiriza pake iwo amakakhala pamodzi ndi anthu akufa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ici ndi coipa m'zonse zicitidwa pansi pano, cakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udio, ndipo misala iri m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.