Ecclesiastes 9:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chikondi chao, chidani chao ndi nsanje yao, zonse zidatha kale. Ndipo pa zonse zochitika pansi pano sadzalandirako kanthu konse mpakampaka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chikondi chao ndi mdano wao ndi dumbo lao lomwe zatha tsopano; ndipo nthawi yamuyaya sagawa konse kanthu kalikonse kachitidwe pansi pano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chikondi chawo, chidani chawo ndiponso nsanje yawo, zonse zinatha kalekale; sadzakhalanso ndi gawo pa zonse zochitika pansi pano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cikondi cao ndi mdano wao ndi dumbo lao lomwe zatha tsopano; ndipo nthawi yamuyaya sagawa konse kanthu kali konse kacitidwa pansi pano.