Ecclesiastes 9:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uzikondwerera moyo pamodzi ndi mkazi amene umamkonda, pa masiku onse a moyo wako wopandapakewu umene Mulungu wakupatsa pansi pano. Ndi zokhazo zimene ungaziyembekeze pa moyo wako ndiponso pa ntchito zako zolemetsa zimene umazigwira pansi pano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wachabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse achabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'ntchito zimene uvutika nazo pansi pano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uzikondwerera moyo pamodzi ndi mkazi wako amene umamukonda, masiku onse a moyo uno wopanda phindu, amene Mulungu wakupatsa pansi pano. Pakuti mkaziyo ndiye gawo la moyo wako pa ntchito yako yolemetsa pansi pano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wacabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse acabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'nchito zimene ubvutika nazo pansi pano.