Ephesians 1:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja Mulungu amaongolera zinthu zonse monga momwe Iye wafunira ndi m'mene watsimikizira. Iye adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale akeake. Adazikonzeratu kuti ziyenera kukhala choncho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa Iye tinayesedwa cholowa chake, popeza tinakonzekeratu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye wakuchita zonse monga mwa uphungu wa chifuniro chake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anatisankhiratu mwa Khristu, atatikonzeratu molingana ndi machitidwe a Iye amene amachititsa zinthu zonse kuti zikwaniritse cholinga cha chifuniro chake,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa iye tinayesedwa colowa cace, popeza tinakonzekeratu monga mwa citsimikizo mtima ca iye wakucita zonse monga mwa uphungu wa cifuniro cace;