Ephesians 1:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, ndi kumkhulupirira Iye, munasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo inunso pamene munamva mawu a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, munayikidwanso mwa Khristu. Mutakhulupirira, anakusindikizani chizindikiro pokupatsani Mzimu Woyera amene Iye analonjeza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a coonadi, Uthenga Wabwino wa cipulumutso canu; ndi kumkhulupirira iye, munasindikizidwa cizindikilo ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,