Ephesians 2:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu amene mtundu wanu sindinu Ayuda, kumbukirani m'mene munaliri kale. Ayuda amadzitchula oumbala, chifukwa cha mwambo umene amachita pa thupi lao, ndipo inu amakutchulani osaumbala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo kumbukirani, kuti kale inu amitundu m'thupi, otchedwa kusadulidwa ndi iwo otchedwa mdulidwe m'thupi, umene udachitika ndi manja;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chake kumbukirani kuti poyamba inu amene munali anthu a mitundu ina mwachibadwa ndipo munkatchedwa “osachita mdulidwe” ndi amene amadzitcha okha “a mdulidwe” (zimene zinachitika mʼthupi ndi manja a anthu).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo kumbukirani, kuti kale inu amitundu m'thupi, ochedwa kusadulidwa ndi iwo ochedwa mdulidwe m'thupi, umene udacitika ndi manja;