Ephesians 2:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono kumbukirani kuti nthaŵi imene ija munali opanda Khristu. Munali alendo, ndipo simunali a mtundu wa anthu osankhidwa ndi Mulungu. Munali opanda gawo pa zimene Mulungu, mwa zipangano zake, adaalonjeza anthu ake. Munkakhala pansi pano opanda chiyembekezo, opandanso Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti nthawi ija munali opanda Khristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israele, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumbukirani kuti nthawi imene inu munali wopanda Khristu, simunkawerengedwa ngati nzika za Israeli ndipo munali alendo pa pangano la lonjezo, wopanda chiyembekezo ndi opanda Mulungu mʼdziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti nthawi ija munali opanda Kristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israyeli, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda ciyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi.