Ephesians 2:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imene ija ifenso tonse tinali ndi moyo wonga wao, ndipo tinkatsata zilakolako za khalidwe lathu lokonda zoipa. Tinkachitanso zilizonse zimene matupi athu ndi maganizo athu ankasirira. Nchifukwa chake, mwachibadwa chathu, tinali oyenera mkwiyo wa Mulungu, monga anthu ena onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi ina tonsefe tinalinso ndi moyo wonga wawo, tinkachitanso zilizonse zimene matupi ndi maganizo athu ankafuna. Mwachibadwa chathu, tinali oyenera chilango monga anthu ena onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu, ndi kucita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo cibadwire, monganso otsalawo;