Ephesians 3:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adandipatsanso ntchito yofotokozera anthu onse za m'mene Mulungu adzachitira zonse zimene Iye adakonzeratu mwa chinsinsi chake. Mulungu amene adalenga zonse, adasunga chinsinsichi chikhalire, nthaŵi isanayambe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kuwalitsira onse adziwe makonzedwe a chinsinsicho, chimene chinabisika kuyambira kalekale mwa Mulungu wolenga zonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinasankhidwa kuti ndifotokoze momveka bwino kwa munthu aliyense za chinsinsi chimenechi, chinsinsi chimene kuyambira kale chinali chobisika mwa Mulungu amene analenga zinthu zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kuwalitsira onse adziwe makonzedwe a cinsinsico, cimene cinabisika ku yambira kale kale mwa Mulungu wolenga zonse;