Ephesians 4:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sitidzakhalanso ngati ana akhanda ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, ndiponso otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya zophunzitsa za anthu onyenga amene amasokeretsa anthu ndi kuchenjera kwao
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero sitidzakhalanso makanda, ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso ndi kuchenjera kwa anthu achinyengo amene amasocheretsa anthu ndi kuchenjera kwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengeka-tengeka ndi mphepo yonse ya ciphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kucenjerera kukatsata cinyengo ca kusoceretsa;