Ephesians 4:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
umene umalamula thupi lonse, ndi kulilumikiza pamodzi ndi mfundo zake zonse. Motero chiwalo chilichonse chimagwira ntchito yake moyenera, ndipo thupi lonse limakula ndi kudzilimbitsa ndi chikondi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuchokera mwa Iye thupi lonse, lolukidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwa Iye thupi lonse lalumikizidwa ndi kugwirana pamodzi ndi mitsempha yothandizira. Likukula ndi kudzilimbitsa lokha mwachikondi, pomwe chiwalo chilichonse chikugwira ntchito yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kucokera mwa Iye thupi lonse, lokowanidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kucititsa kwa ciwalo conse pa muyeso wace, licita makulidwe a thupi, kufikira cimango cace mwa cikondi.