Ephesians 4:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼkamwa mwanu musatuluke mawu aliwonse onyansa, koma okhawo amene ndi othandiza kulimbikitsa ena molingana ndi zosowa zawo, kuti athandize amene akawamve.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
8 Nkhani yonse yobvunda isaturuke m'kamwa mwanu, koma ngati pali yina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, 9 kuti ipatse cisomo kwa iwo akumva.