Ephesians 5:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adafuna kuti akauimike pamaso pake uli waulemerero, wopanda banga kapena makwinya, kapena kanthu kena kalikonse kouipitsa, koma uli woyera ndi wangwiro kotheratu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti Iye akadziikire yekha Mpingo wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda chilema.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anachita zimenezi kuti awupereke mpingowo kwa Iye mwini, mpingo wowala ndi waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapena chilema chilichonse, koma oyera ndi wangwiro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kutilye akadziikire yekha Eklesia wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda cirema.