Ephesians 5:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Popeza kuti ndinu anthu a Mulungu, ndiye kuti dama kapena zonyansa, kapena masiriro oipa zisatchulidwe nkomwe pakati panu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma dama ndi cidetso conse, kapena cisiriro, zisachulidwe ndi kuchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;