Ephesians 6:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa kwambiri lifika, mudzathe kuyima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzayimabe mwamphamvu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa ici mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima citsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutacita zonse, mudzacirimika.