Ephesians 6:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono imani mwamphamvu, mutamangira choonadi ngati lamba mʼchiwuno mwanu, mutavala chilungamo ngati chitsulo chotchinjiriza pa chifuwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace cirimikani, mutadzimangira m'cuuno mwanu ndi coonadi, mutabvalanso capacifuwa ca cilungamo;